MUREA COOKSTOVE PROJECT

By Arnold Kadziponye

Mbaula ya Chitetezo ingaoneke ngati chinthu chosathandiza kapena tinene kuti chopanda ntchito kwenikweni, koma ili ndi ubwino wambiri ndipo ndiyothandiza kuposa monga tingaganizire. Kuonongeka kwa chilengedwe makamaka mitengo ndivuto lalikulu kuno ku Malawi chifukwa pafupifupi 97% ya mabanja athu amagwiritsa ntchito nkhuni pophikira ndi zina zotero. Ndipo Malawi ndi dziko limene zachilengedwe zikuonongeka mofulumira kwambiri mu chigawo chino cha kummwera kuposa dziko lina lililonse. Kuonongeka kwa zachilengedwe kwapangitsanso kuti kukongola kwa dziko lathu kukhudzidwe, komanso pali mavuto ena ambiri omwe adza Kamba kavutoli.

Mitengo imabweretsa m’phweya wabwino, imathandiza kuchepetsa kukokoloka kwa nthaka zomwe zimabweretsa kusefuka kwa madzi, komanso mitengo imathandiza kuti mbewu zikule bwino. Monga ndanena kale kuti pafupifupi 97% ya anthu m’dziko lino amadalira ntchito nkhuni kuti athe kuphika chakudya chawo, enanso amagwiritsa ntchito Makala. Kugwiritsa ntchito nkhuni kapena Makala silingakhale vuto lalikulu palokha popeza izi ndi zina mwa mphamvu za m’bwezera (zingathe kubwezeretsedwa), koma ngati dziko sitikugwiritsa bwino ntchito zinthu izi pofna kuti tikhale tikugwiritsabe kwa nthawi yaitali mpaka kale. Mbaula monga ya Chitetezo zingakhale yankho popeza zimagwiritsa ntchito nkhuni zochepa poyerekeza ndi mafuwa atatu, mbaula zina zimatha kugwiritsa ntchito ma briquettes

Njira zophikira zamakolo zimatulutsanso utsi wambiri omwe umapereka chiopysezo pa moyo wamunthu. Imfa zambiri zikudza kamba ka utsi omwe umapumidwa kudzera m’njira yophika pa dziko lonse lapansi. Kuno kwathu ku Malawi pali imfa zokwana 13,000 pa chaka zomwe zimadza kamba kopuma m’pweya oyipawu. Vuto ili lingathe kapena kuchepetsedwa pamene njira zophikira zomwe zikugwiritsidwa ntchito zikutulutsa utsi ochepa komanso polola kuti nkhuni zigwiritsidwe bwino ntchito yake, pogwiritsa ntchito mbaula ngati ya Chitetezo.

Magulu amene bungwe la MuREA lidakhazikitsa m’maboma a Mulanje ndi Phalombe alipo okwana 66 ndipo izi zapangitsa kuti azimai omwe akutenga nawo mbali adzipeza ndalama powumba ndi kugulitsa mbaula zimenezi zomwe zathandiza kuti akhale odzidalira pankhani ya chuma.

“Tisanayambe kupanga mbaula zimenezi, timapita kuphiri kukatolera nkhuni pafupipafupi ndipo mtolo omwe tatola umatha masiku ochepa mwina atatu okha, pamene lero lino mtolo omwewo ukutenga sabata ziwiri zomwe zapangitsa kuti tisunge ndalama komanso kukhala ndi nthawi yokwanira kuchita ntchito zina zachitukuko m’mudzi mwathu” adatero Mai Linly Makupe am’mudzi mwa Demula kwa Mfumu Yaikulu Chikumbu

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *